1 Samuel 9:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo adayankha kuti, “Inde, alipo. Akunka patsogolo panupa. Fulumirani. Wangofika tsopano apa mumzindamu, chifukwa anthu akukapereka nsembe lero ku kachisi ku phiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anawayankha nati, Alipo; onani ali m'tsogolo mwanu; fulumirani pakuti wabwera lero kumudzi kuno; popeza lero anthu akuti aphere nsembe pamsanje;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anayankha, “Inde alipo. Ali kutsogolo kwanuku, fulumirani tsopano, wangobwera kumene mu mzinda wathu uno lero, chifukwa lero anthu akupereka nsembe ku phiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anawayankha nati, Alipo; onani ali m'tsogolo mwanu; fulumirani pakuti wabwera lero kumudzi kuno; popeza lero anthu akuti aphere nsembe pamsanje;