1 Samuel 9:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukangoloŵa mumzindamo, mumpeza asanapite kukachisiko kuti akadye. Anthu sangayambe kudya mpaka iye atabwera, poti ayenera kuyamba waidalitsa nsembeyo. Pambuyo pake ndiye anthu oitanidwa adzayamba kudya. Tsono pitani, mukumana naye posachedwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mutafika m'mudzi, pomwepo mudzampeza, asanakwere kumsanje kukadya; pakuti anthu sadzadya, koma iye atafika ndipo; pakuti iye amadalitsa nsembeyo; ndipo atatero oitanidwawo amadya. Chifukwa chake kwerani; popeza nthawi yino mudzampeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukangolowa mu mzindawo mumupeza asanapite ku phiri kukadya. Anthu sangayambe kudya iye asanabwere chifukwa iyeyu ayenera kudalitsa nsembeyo. Kenaka anthu oyitanidwa adzayamba kudya. Pitani tsopano, chifukwa muyenera kumupeza nthawi ino.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mutafika m'mudzi, pomwepo mudzampeza, asanakwere kumsanje kukadya; pakuti anthu sadzadya, koma iye atafika ndipo; pakuti iye amadalitsa nsembeyo; ndipo atatero oitanidwawo amadya. Cifukwa cace kwerani; popeza nthawi yino mudzampeza.