1 Samuel 9:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Maŵa nthaŵi yonga yomwe ino, ndidzakutumizira munthu wa ku dera la Benjamini, udzamudzoze kuti akhale mfumu ya anthu anga Aisraele. Adzapulumutsa anthu kwa Afilisti. Ndaona kuzunzika kwao, ndipo ndamva kulira kwao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mawa, monga dzuwa lino, ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini, udzamdzoza iye akhale mtsogoleri wa anthu anga Israele, kuti akawapulumutse anthu anga m'manja a Afilisti; pakuti Ine ndinapenya pa anthu anga, popeza kulira kwao kunandifika Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini. Udzamudzoze kuti akhale mtsogoleri wa anthu anga, Aisraeli. Iye adzawapulumutsa mʼdzanja la Afilisti. Ine ndaona kuzunzika kwawo ndipo ndamva kulira kwawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mawa, monga dzuwa lino, ndidzakutumizira munthu wocokera ku dziko la Benjamini, udzamdzoza iye akhale mtsogoleri wa anthu anga Israyeli, kuti akawapulumutse anthu anga m'manja a Afilisti; pakuti Ine ndinapenya pa anthu anga, popeza kulira kwao kunandifika Ine.