1 Samuel 9:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musadandaule za abulu anu amene akhala akusoŵa masiku atatu apitaŵa, poti adapezeka kale. Kodi ndani amene Aisraele akumfunitsitsa? Kodi sindiwe ndi banja lonse la bambo wako?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Za abulu ako atatayika adapita masiku atatu, usalingalirenso iwowa; pakuti anapezedwa. Ndipo chifuniro chonse cha Israele chili kwa yani? Si kwa iwe ndi banja lonse la atate wako?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musadere nkhawa za abulu anu amene akhala akusowa masiku atatu apitawa, poti apezeka kale. Kodi Aisraeli onse akufunitsitsa ndani? Kodi si ndiwe ndi nyumba yonse ya abambo ako?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Za aburu ako atatayika adapita masiku atatu, usalingalirenso iwowa; pakuti anapezedwa. Ndipo cifuniro conse ca Israyeli ciri kwa yani? Si kwa iwe ndi banja lonse la atate wako?