1 Samuel 9:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Saulo adayankha kuti, “Komatu ine ndine Mbenjamini, fuko laling'ono pakati pa mafuko onse a Aisraele. Kodi banja langa sindiye laling'ono kwambiri pakati pa mabanja a fuko la Benjamini? Chifukwa chiyani mukundilankhula zotere?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo anayankha nati, Sindili Mbenjamini kodi wa fuko laling'ono mwa Israele? Ndiponso banja lathu nlochepa pakati pa mabanja onse a fuko la Benjamini? Potero mulankhula bwanji mau otere ndi ine?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli anayankha, “Inetu ndine Mbenjamini, fuko lalingʼono la mafuko onse a Israeli, ndipo banja langa ndi lalingʼono pakati pa mabanja a fuko la Benjamini. Nanga nʼchifukwa chiyani mukunena zimenezi kwa ine?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli anayankha nati, Sindiri Mbenjamini kodi, wa pfuko laling'ono mwa Israyeli? Ndiponso banja lathu nlocepa pakati pa mabanja onse a pfuko la Benjamini? Potero mulankhula bwanji mau otere ndi ine?