1 Samuel 9:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho wophika uja adatenga mwendo wa nyama naupereka kwa Saulo. Ndipo Samuele adati, “Nayi nyama imene ndidaakusungira. Idya, chifukwa ndidaakuikira padera kuti pa nthaŵi yake ino, uidye pamodzi ndi anthu amene ndidaŵaitana.” Choncho Saulo adadya ndi Samuele tsiku limenelo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wophikayo ananyamula mwendo ndi mnofu wake, nauika pamaso pa Saulo. Ndipo Samuele anati, Onani chimene tinakuikirani? Muchiike pamaso panu, nudye; pakuti ichi anakuikirani kufikira nthawi yonenedwa, popeza ndinati, Ndinaitana anthuwo. Chomwecho Saulo anadya ndi Samuele tsiku lija.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero wophikayo anatenga mwendo wa nyama ndipo anawuyika patsogolo pa Sauli. Samueli anati “Nayi nyama imene ndinakusungira kuti pa nthawi yake udye pamodzi ndi anthu amene ndawayitana.” Ndipo Sauli anadya tsiku limenelo ndi Samueli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wophikayo ananyamula mwendo ndi mnofu wace, nauika pamaso pa Sauli. Ndipo Samueli anati, Onani cimene tinakuikirani muciike pamaso panu, nudye; pakuti ici anakuikirani kufikira nthawi yonenedwa, popeza ndinati, Ndinaitana anthuwoo Comweco Sauli anadya ndi Samueli tsiku lija.