1 Samuel 9:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mbandakucha Samuele adaitana Saulo padengapo kuti, “Dzuka, ndikuperekeze, ndikutule apo.” Pompo Saulo adadzuka, ndipo onse aŵiriwo adakaloŵa mu mseu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anauka mamawa; ndipo kutacha, Samuele anaitana Saulo ali pamwamba pa nyumba, nati, Ukani kuti ndikuloleni mumuke. Ndipo Saulo anauka, natuluka onse awiri, iye ndi Samuele, kunka kunja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mʼbandakucha Samueli anayitana Sauli pa dengapo nati, “Konzeka ndipo ine ndikuperekeza.” Choncho Sauli anadzuka ndipo onse awiri, Samueli ndi Sauli anakalowa mu msewu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anauka mamawa; ndipo kutaca, Samueli anaitana Sauli ali pamwamba pa nyumba, nati, Ukani kuti ndikuloleni mumuke. Ndipo Sauli anauka, naturuka onse awiri, iye ndi Samueli, kunka kunja.