1 Samuel 9:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atafika kothera kwake kwa mzindawo, Samuele adauza Saulo kuti, “Uza mnyamatayu kuti abatsogola, iwe wekha uime pang'ono, kuti ndikuuze mau ochokera kwa Mulungu.” Mnyamata uja adatsogola.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene analikutsika polekeza mudzi, Samuele ananena ndi Saulo, Uzani mnyamatayo abatsogola; napita iyeyo. Koma inu muime pano, kuti ndikumvetseni mau a Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atakafika ku mathero a mzindawo, Samueli anati kwa Sauli, “Muwuzeni mnyamata wanu kuti atsogole, koma inuyo muyime pangʼono kuti ndikuwuzeni mawu ochokera kwa Mulungu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene analikutsika polekeza mudzi, Samueli ananena ndi Sauli, Uzani mnyamatayo abatsogola; napita iyeyo. Koma inu muime pano, kuti ndikumvetseni mau a Mulungu.