1 Samuel 9:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina Kisi adaona kuti abulu ake asoŵa. Choncho adauza Saulo kuti, “Tenga mmodzi mwa anyamata antchitoŵa, munyamuke, mukaŵafunefune abuluwo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo abulu a Kisi, atate wa Saulo, analowerera. Ndipo Kisi anati kwa Saulo mwana wake, Utenge mnyamata mmodzi, nunyamuke, kukafuna abuluwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono abulu a Kisi, abambo ake a Sauli anasowa. Choncho Kisi anati kwa mwana wake Sauli, “Tenga wantchito mmodzi ndipo mupite mukafunefune abuluwo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo aburu a Kisi, atate wa Sauli, analowerera. Ndipo Kisi anati kwa Sauli mwana wace, Utenge mnyamata mmodzi, nunyamuke, kukafuna aburuwo.