1 Samuel 9:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo adabzola dziko lamapiri la Efuremu ndi la Salisa, koma osaŵapeza. Kenaka adabzola dziko la Salimu, koma kumeneko kunalibenso. Adabzolanso dziko la Benjamini, koma osaŵapezabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapyola dziko lamapiri la Efuremu, napyola dziko la Salisa, koma sanawapeze; pamenepo anapyolanso dziko la Salimu, koma panalibe pamenepo, napyola dziko la Abenjamini, osawapeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho iwo anadutsa dziko la mapiri a Efereimu ndi dera la Salisa, koma sanawapeze. Anadutsa ku Saalimu koma abuluwo sanawapeze. Kenaka anadutsa dziko la Benjamini, koma osawapezabe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapyola dziko lamapiri la Efraimu, napyola dziko la Salisa, koma sanawapeza; pamenepo anapyolanso dziko la Salimu; koma panalibe pamenepo, napyola dziko la Abenjamini, osawapeza.