1 Samuel 9:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atafika ku dziko la Zufu, Saulo adauza mnyamata wake amene anali naye kuti, “Tiye tizibwerera, kuwopa kuti bambo wanga angaleke kusamala za abulu ndi kudera nkhaŵa za ife.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene anafika ku dziko la Zufu, Saulo anamuuza mnyamata amene anali naye, kuti, Tiye tibwerere; kuti atate wanga angaleke kusamalira abuluwo, ndi kutenga nkhawa chifukwa cha ife.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika ku dera la Zufi, Sauli anawuza mnyamata wake kuti, “Tiye tibwerere, mwina abambo anga angasiye kudandaula za abulu ndipo adzayamba kudandaula za ife.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene anafika ku dziko la Zufi, Sauli anamuuza mnyamata amene anali naye, kuti, Tiye tibwerere; kuti atate wanga angaleke kusamalira aburuwo, ndi kutenga nkhawa cifukwa ca ife.