1 Samuel 9:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mnyamatayo adati, “Mumzindamu muli munthu wa Mulungu, munthu amene onse amamchitira ulemu. Zonse zimene amanena zimachitikadi. Bwanji tipite kumeneko. Mwina mwake angathe kutiwuza za ulendo wathuwu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ananena naye, Onatu, m'mudzi muno muli munthu wa Mulungu, ndiye munthu anthu amchitira ulemu; zonse azinena zichitika ndithu; tiyeni tipite komweko, kapena adzakhoza kutidziwitsa zimene tili kuyendera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mnyamatayo anayankha kuti, “Taonani, mu mzinda uwo muli munthu wa Mulungu. Anthu amamupatsa ulemu kwambiri, ndipo zonse zimene amanena zimachitika. Tiyeni tipite kumeneko tsopano. Mwina adzatiwuza kumene tiyenera kulowera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ananena naye, Onatu, m'mudzi muno muli munthu wa Mulungu, ndiye munthu anthu amcitira ulemu; zonse azinena zicitika ndithu; tiyeni tipite komweko, kapena adzakhoza kutidziwitsa zimene tirikuyendera.