1 Samuel 9:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Saulo adafunsa mnyamata wakeyo kuti, “Tsono tikapita, timtengere chiyani munthuyo? Buledi amene adaali m'matumba mwathu watha, ndipo tilibe ndi mphatso yomwe yoti tingampatse munthu wa Mulunguyo. Kodi tili ndi chiyani?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo ananena ndi mnyamata wake, Koma taona, tikapitako timtengere chiyani munthuyo? Popeza mkate udatha m'zotengera zathu, ndiponso tilibe mphatso yakumtengera munthu wa Mulungu, tili nacho chiyani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli anafunsa mnyamata wake kuti, “Tikapita tikamupatsa chiyani munthuyo pakuti chakudya chimene chinali mʼmatumba mwathu chatha? Tilibe mphatso iliyonse yoti timutengere munthu wa Mulungu. Nanga tili ndi chiyani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli ananena ndi mnyamata wace, Koma taona, tikapitako nmtengere ciani munthuyo? popeza mkate udatha m'zotengera zathu, ndiponso tiribe mphatso yakumtengera munthu wa Mulungu, tiri naco ciani?