1 Samuel 9:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mnyamatayo adayankha kuti, “Pano ndili ndi kandalama kakang'ono kasiliva, ndipo ndikapereka kwa munthu wa Mulunguyo, kuti atiwuze kumene kwapita abuluwo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mnyamatayo anayankhanso kwa Saulo nati, Onani m'dzanja langa muli limodzi la magawo anai a sekeli wa siliva; ndidzampatsa munthu wa Mulungu limeneli kuti atiuze njira yathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mnyamatayo anayankha kuti, “Onani, ndili ndi kandalama kakangʼono ka siliva. Ndikamupatsa munthu wa Mulunguyo ndipo akatidziwitsa kumene kuli abuluwo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mnyamatayo anayankhanso kwa Sauli nati, Onani m'dzanja langa muli limodzi la magawo anai a sekeli wa siliva; ndidzampatsa munthu wa Mulungu limeneli kuti atiuze njira yathu.