1 Thessalonians 1:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja Uthenga Wabwino umene tidadza nawo kwa inu sunali wapakamwa chabe, koma tinkaulalika ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndiponso mosakayika konse. Mukudziŵa m'mene tinkakhalira pakati panu pofuna kuti tikuthandizeni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti Uthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m'mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m'kuchuluka kwakukulu; monga mudziwa tinakhala onga otani mwa inu chifukwa cha inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
chifukwa uthenga wathu wabwino sunafike kwa inu ndi mawu okha, koma ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndi chitsimikizo chachikulu. Mukudziwa mmene tinkakhalira pakati panu kuti tikuthandizeni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti Vthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m'mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m'kucuruka kwakukuru; monga mudziwa tinakhala onga otani mwa inu cifukwa ca inu.