1 Thessalonians 1:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inde kuchokera kwa inu mau a Ambuye adakafika ku Masedoniya ndi ku Akaiya, ndipo kuwonjezera apo mbiri yakuti mudakhulupirira Mulungu idawanda ponseponse. Motero palibe chifukwa chakuti ife nkunenapo kanthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti kutuluka kwa inu kudamveka mau a Ambuye, osati m'Masedoniya ndi Akaya mokha, komatu m'malo monse chikhulupiriro chanu cha kwa Mulungu chidatuluka; kotero kuti sikufunika kwa ife kulankhula kanthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera kwa inu, uthenga wa Ambuye unamveka ku Makedoniya ndi ku Akaya ndipo mbiri ya chikhulupiriro chanu mwa Mulungu yamveka ponseponse. Choncho sikofunikanso kuti tinene kanthu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti kuturuka kwa inu kudamveka mau a Ambuye, osati m'Makedoniya ndi Akaya mokha, komatu m'malo monse cikhulupiriro canu ca kwa Mulungu cidaturuka; kotero kuti sikufunika kwa ife kulankhula kanthu.