1 Thessalonians 1:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo amakamba okha za m'mene mudatilandirira, ndi za m'mene mudasiyira mafano ndi kutembenukira kwa Mulungu weniweni wamoyo, kuti muzimtumikira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti iwo okha alalikira za ife, malowedwe athu a kwa inu anali otani; ndi kuti munatembenukira kwa Mulungu posiyana nao mafano, kutumikira Mulungu weniweni wamoyo,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pakuti iwo amafotokoza za momwe munatilandirira. Iwo amatiwuza za momwe munatembenukira kwa Mulungu kusiya mafano ndi kutumikira Mulungu wamoyo ndi woona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti iwo okha alalikira za ife, malowedwe athu a kwa inu anali otani; ndi kuti munatembeoukira kwa Mulungu posiyana nao mafano, kutumikira Mulungu weni weni wamoyo,