1 Thessalonians 2:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abale, zimene zidakugwerani inu ndi zomwe zidagweranso mipingo ya Mulungu ya mwa Khristu Yesu imene ili ku Yudeya. Paja inunso anthu akwanu adakuzunzani monga momwe Ayuda adazunzira akhristu a ku Yudeya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti inu, abale, munayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala m'Yudeya mwa Khristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva kowawa ndinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowa pa manja a Ayuda;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti inu abale, munakhala otsanzira mipingo ya Mulungu ya ku Yudeya, imene ili mwa Khristu Yesu. Munasautsidwa kuchokera kwa anthu a mtundu wanu, zinthu zomwezo zimene mipingo imeneyi inasautsidwa ndi Ayuda,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti inu, abale, munayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala m'Yudeya mwa Kristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva kowawa nelinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowapa manja a Ayuda;