1 Thessalonians 2:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwowotu amatiletsa kulalika Uthenga Wabwino kwa anthu a mitundu ina woŵathandiza kuti apulumuke. Motero nthaŵi zonse amanka nawonjezerawonjezera machimo ao, mwakuti tsopano mkwiyo wa Mulungu waŵagwera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
natiletsa ife kuti tisalankhule ndi akunja kuti apulumutsidwe; kudzaza machimo ao nthawi zonse; koma mkwiyo wafika pa iwo kufikira chimaliziro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndikutiretsa ife kuti tisayankhule ndi a mitundu ina kuti angapulumuke. Motero iwo amadziwunjikira okha machimo awo. Mkwiyo wa Mulungu wa afikira tsopano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
natiletsa ife kuti tisalankhule ndi akunja kuti apulumutsidwe; kudzaza macimo ao nthawi zonse; koma mkwiyo wafika pa iwo kufikira cimariziro.