1 Thessalonians 2:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abale, pamene tidasiyana nanu ngakhale kanthaŵi pang'ono, tinkalakalaka kwambiri kuwonana nanunso maso ndi maso. Ngakhale tinkachoka, mtima wathu unali nanube.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ife, abale, angakhale adatichotsa kusiyana nanu kanthawi, osapenyana maso, koma kusiyana mtima ai, tinayesetsa koposa kuona nkhope yanu ndi chilakolako chachikulu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma abale, titasiyana kwa nthawi pangʼono (mʼthupi osati mʼmaganizo), tinayesetsa koposa kuti tikuoneni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ife, abale, angakhale adaticotsa kusiyana nanu kanthawi, osapenyana maso, koma kusiyana mtima ai, tinayesetsa koposa kuona nkhope yanu ndi cilakolako cacikuru;