1 Thessalonians 2:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abale, simukumbukira nanga kuti tinkagwira ntchito kwambiri mpaka kutopa? Monse muja tinkakulalikirani Uthenga Wabwino wa Mulungu, tinkagwira ntchito zamanja usana ndi usiku, kuwopa kuti tingavutitse wina aliyense mwa inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mukumbukira, abale, chigwiritso chathu ndi chivuto chathu; pochita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale, pakuti mukumbukira kugwira ntchito kwathu kwambiri ndi kuvutika; ife tinagwira ntchito usana ndi usiku ndi cholinga chakuti tisakhale cholemetsa, kwa aliyense pamene ife tinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mukumbukila, abale, cigwiritso cathu ndi cibvuto cathu; pocita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu.