1 Thessalonians 3:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake, pamene sindidathenso kupirira, ndidatuma Timoteo kuti adzaone m'mene chiliri chikhulupiriro chanu. Pakuti ndinkaopa kuti kapena Satana, Wonyenga uja, adakunyengani, ndipo kuti ntchito zathu zonse pakati panupo zidangopita pachabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa ichi inenso, posalekereranso, ndinatuma kukazindikira chikhulupiriro chanu, kuti kapena woyesa akadakuyesani, ndipo chivuto chathu chikadakhala chopanda pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake, pamene sindikanathanso kupirira, ndinatuma Timoteyo kuti adzaone mmene chikhulupiriro chanu chilili. Ndinkaopa kuti mwina wonyengayo, wakunyengani mʼnjira ina yake ndi kuti ntchito zathu zasanduka zosapindula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa ici inenso, posalekereranso, ndinatuma kukazindikira cikhulupiriro canu, kuti kaperta: woyesa akadakuyesani, ndipo cibvuto cathu cikadakhala copanda pace.