1 Thessalonians 3:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsopano Timoteo wabwerako kuchokera kwanuko, ndipo watisimbira mbiri yokoma ya chikhulupiriro chanu ndi chikondi chanu. Watiwuzanso kuti masiku onse mumatikumbukira mokondwa, ndipo kuti mumalakalaka kutiwona ife, monga momwe ifeyo timafunitsitsira kukuwonaninso inuyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma tsopano pofika Timoteo kwathu kuchokera kwa inu, ndi kutifotokozera mbiri yokoma ya chikhulupiriro ndi chikondano chanu, ndi kuti mutikumbukira bwino masiku onse, pokhumba kutiona ife, monganso ife kukuonani inu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma tsopano Timoteyo wabwera kuchokera kwanuko ndipo watibweretsera nkhani yabwino ya chikhulupiriro chanu ndi chikondi chanu. Iye watiwuzanso kuti masiku onse mumatikumbukira mokondwa, ndipo kuti mumafunitsitsa kutionanso, monga momwe ifenso timalakalakira kukuonani inuyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma tsopano pofika Timoteo kwathu kucokera kwa inu, ndi kutifotokozera mbiri yokoma ya cikhulupiriro ndi cikondano canu, ndi kuti mutikumbukila bwino masiku onse, pokhumba kutiona ife, monganso ire kukuonani inu;