1 Thessalonians 4:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano tikuuzeni mau a Ambuye mwini. Ife amoyofe, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sikuti tidzaŵasiya kumbuyo amene adamwalira aja ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ichi tinena kwa inu m'mau a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Molingana ndi mawu a Ambuye mwini, tikukuwuzani kuti, ife amene tikanali ndi moyo, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sitidzawasiya kumbuyo amene anagona kale.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ici tinena kwa inu m'mau a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo.