1 Thessalonians 5:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onetsetsani kuti wina aliyense mnzake akamchita choipa, asabwezere choipacho. Koma nthaŵi zonse muziyesetsa kuchitira zabwino anzanu ndi anthu ena onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Penyani kuti wina asabwezere choipa womchitira choipa; komatu nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onetsetsani kuti wina asabwezere choyipa kwa omuchitira choyipa koma nthawi zonse yesetsani kukhala okoma mtima kwa wina ndi mnzake; ndiponso ndi kwa anthu ena onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Penyani kuti wina asabwezere coipa womcitira coipa; komatu nthawi zonse mutsatire cokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.