1 Thessalonians 5:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene anthu azikati, “Pali mtendere, tili pabwino”, pamenepo chiwonongeko chidzaŵagwera modzidzimutsa. Chidzaŵadzidzimutsa monga momwe zoŵaŵa zimamchitira mkazi pa nthaŵi yoti achire; ndipo sadzatha konse kuchizemba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene anthu akunena kuti, “Mtendere ndi chitetezo,” chiwonongeko chidzafika pa iwo mwadzidzidzi, monga zowawa za amayi pobereka, ndipo sadzathawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo cionongeko cobukapo cidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.