1 Thessalonians 5:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ife, popeza kuti zathu nzausana, tisamaledzera. Tikhale titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala chachitsulo chapachifuwa. Ndipo ngati chisoti choteteza kumutu tivale chiyembekezo chakuti tidzapulumuka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ife popeza tili a usana tisaledzere, titavala chapachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi; ndi chisoti chili chiyembekezo cha chipulumutso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma popeza ndife a usana, tikhale odzisunga, titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala pachifuwa, ndi chiyembekezo cha chipulumutso ngati chipewa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ife popeza tiri a usana tisaledzere, titabvala capacifuwa ca cikhulupiriro ndi cikondi; ndi cisoti ciri ciyembekezo ca cipulumutso.