1 Timothy 1:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ngakhale kuti kale ndinkamuchita chipongwe, kumzunza ndi kumnyoza. Koma Mulungu adandichitira chifundo chifukwa ndinkazichita mosadziŵa, poti ndinali wopanda chikhulupiriro.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; komatu anandichitira chifundo, popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale kuti kale ndinali wachipongwe, wozunza ndi wankhanza, anandichitira chifundo chifukwa ndinkachita mwaumbuli ndi mopanda chikhulupiriro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wacipongwe; komatu anandicitira cifundo, popeza ndinazicita wosazindikira, wosakhulupirira;