1 Timothy 1:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uŵauze kuti aleke kumangoika mtima pa nthano zopeka, ndi pa kufufuza kosalekeza dongosolo la maina a makolo. Zimenezi zimangoutsa mikangano chabe, siziphunzitsa konse zimene Mulungu adakonzeratu, zomwe zimadziŵika pakukhulupirira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kapena asasamale nkhani zachabe, ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, ndiwo akuutsa mafunso, osati za udindo wa Mulungu umene uli m'chikhulupiriro;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kapena kumangoyika mitima pa nthano zopeka ndi kufufuza za mayina a makolo awo. Zinthu zotere zimapititsa mʼtsogolo mikangano mʼmalo mwa ntchito ya Mulungu yomwe ndi ya chikhulupiriro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kapena asasamale nkhani zacabe, ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, ndiwo akuutsa mafunso, osati za udindo wa Mulungu umene uli m'cikhulupiriro;