1 Timothy 1:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mumvetsetse kuti saika malamulo chifukwa cha anthu olungama, koma chifukwa cha anthu osamvera, ndi osaweruzika, anthu ochimwa ndi osapembedza, monga anthu opha atate ao, amai ao, kapena anthu ena.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
podziwa ichi, kuti lamulo siliikika kwa munthu wolungama, koma kwa osaweruzika ndi osamvera lamulo, osapembedza, ndi ochimwa, osalemekeza ndi amnyozo, akupha atate ndi akupha amai, akupha anzao,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tikudziwanso kuti Malamulo sakhazikitsidwa chifukwa cha anthu olungama, koma ophwanya lamulo ndi owukira, osaopa Mulungu ndi ochimwa, wopanda chiyero ndi osapembedza; amene amapha abambo awo ndi amayi awo, kapena anthu ena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
podziwa ici, kuti lamulo siliikika kwa munthu wolungama, koma kwa osayeruzika ndi osamvera lamulo, osapembedza, ndi ocimwa, osalemekeza ndi amnyozo, akupha atate ndi akupha amai, akupha anzao,