1 Timothy 2:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo adadzipereka kuti akhale momboli wa anthu onse. Umenewu unali umboni umene udaperekedwa pa nthaŵi yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene anadzipereka yekha chiombolo m'malo mwa onse; umboni m'nyengo zake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iyeyu anadzipereka kukhala dipo lowombolera anthu onse. Umenewu ndi umboni umene waperekedwa mu nthawi yake yoyenera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene anadzipereka yekha ciombolom'malo mwa onse; umboni m'nyengo zace;