1 Timothy 2:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake ine adandiika kuti ndikhale mlaliki wake ndiponso mtumwi, wophunzitsa anthu a mitundu ina mau a chikhulupiriro choona. Sindikunamatu ai, ndikunena zoona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
umene anandiika ine mlaliki wake ndi mtumwi (ndinena zoona, wosanama ine), mphunzitsi wa amitundu m'chikhulupiriro ndi choonadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake anandisankha kukhala mlaliki ndiponso mtumwi wophunzitsa anthu a mitundu ina mawu achikhulupiriro choona. Sindikunama ayi, ndikunena zoona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
umene anandiika ine mlaliki wace ndi mtumwi (ndinena zoona, wosanama ine), mphunzitsi wa amitundu m'cikhulupiriro ndi coonadi.