1 Timothy 2:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikufunanso kuti akazi azivala mwaulemu, mwanzeru ndi moyenera. Inde adzikongoletse, komatu osati ndi tsitsi lochita kukonza monyanyira, kapena ndi zokongoletsa zagolide, kapena mikanda yamtengowapatali, kapena zovala zamtengowapatali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemonso, akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golide kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikufunanso kuti amayi azivala mwaulemu, modzilemekeza ndi moyenera. Adzikongoletse koma osati ndi tsitsi loluka mowonjeza muyeso kapena zokongoletsa zagolide kapena mikanda yamtengowapatali kapena ndi zovala zamtengowapatali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemonso, akazi adzibveke okha ndi cobvala coyenera, ndi manyazi, ndi cidziletso; osati ndi tsitsi lace loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena maraya a mtengo wace wapatali;