1 Timothy 3:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwonso ayambe ayesedwa, ndipo pambuyo pake, ngati alibe chokayikitsa, ndiye asenze udindo wa atumiki.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iwonso ayamba ayesedwe; pamenepo atumikire, akakhala opanda chifukwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ayambe ayesedwa kaye, ndipo ngati palibe kanthu kowatsutsa, aloleni akhale atumiki.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iwonso ayambe ayesedwe; pamenepo atumikire, akakhala opanda cifukwa.