1 Timothy 3:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithudi, chinsinsi cha chipembedzo chathu nchachikulu: “Iye uja adaonekera ali ndi thupi la munthu, Mzimu Woyera adamchitira umboni kuti ndi wolungama, angelo adamuwona, adalalikidwa pakati pa anthu a mitundu yonse, anthu a pa dziko lonse lapansi adamkhulupirira, Iyeyo adatengedwa kunka kumwamba mu ulemerero.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa m'ulemerero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mosakayikira, chinsinsi cha chikhulupiriro chathu chachikulu: Khristu anaonekera ali ndi thupi la munthu, Mzimu anamuchitira umboni, angelo anamuona, analalikidwa pakati pa mitundu yonse, dziko lapansi linamukhulupirira, anatengedwa kupita kumwamba mwa ulemerero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pobvomerezeka, cinsinsi ca kucitira Mulungu ulemu ncacikuru: iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa m'ulemerero.