1 Timothy 4:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mzimu Woyera akunena momveka kuti pa masiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chao. Adzamvera mizimu yonyenga ndi zophunzitsa zochokera kwa mizimu yoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m'masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mzimu akunena momveka bwino kuti mʼmasiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chawo ndi kutsatira mizimu yonyenga ndi zinthu zophunzitsidwa ndi ziwanda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m'masiku otsiriza ena adzataya cikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosoceretsa ndi maphunziro a ziwanda,