1 Timothy 5:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuwonjezera pamenepo, amagwa m'chizoloŵezi cha kungokhala khale, motero amangoyendayenda ku nyumba za anthu. Tsonotu samangokhala khale chabe ai, amachitanso miseche nkumaloŵera za eni, ndi kukhala omalankhula zimene samayenera kulankhula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo aphunziraponso kuchita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pake, nachita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komanso amakhala ndi chizolowezi cha ulesi ndi kumangoyenda khomo ndi khomo. Ndipo sikungokhala aulesi kokha komanso kuchita miseche, kududukira za eni ake, kumangokamba zinthu zosayenera kukamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo aphunziraponso kucita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pace, nacita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera.