1 Timothy 5:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ngati mai wamasiye ali ndi ana kapena adzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wao pa banja lao moopa Mulungu, kuti pakutero abwezere makolo ao zimene adalandira kwa iwo. Pakuti zimenezi Mulungu amakondwera nazo akamaziwona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati mkazi wamasiye ali ndi ana ndi zidzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wawo pa banja lawo moopa Mulungu, potero akubweza zabwino kwa makolo awo ndi agogo awo. Pakuti zimenezi ndiye zimakondweretsa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kucitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ici ncolandirika pamaso pa Mulungu.