1 Timothy 6:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onse amene ali mu ukapolo aziwona ambuye ao ngati oyenera kuŵachitira ulemu ndithu, kuti anthu anganyoze dzina la Mulungu ndiponso zimene timaphunzitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Onse amene ali akapolo a m'goli, ayesere ambuye a iwo okha oyenera ulemu wonse, kuti dzina la Mulungu ndi chiphunzitso zisachitidwe mwano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onse amene ali mu ukapolo ayenera kuona ambuye awo ngati oyenera kuwachitira ulemu, kuti anthu anganyoze dzina la Mulungu ndi chiphunzitso chathu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Onse amene ali akapolo a m'goli, ayesere ambuye a iwo okha oyenera ulemu wonse, kuti dzina la Mulungu ndi ciphunzitso zisacitidwe mwano.