1 Timothy 6:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu kukonda ndalama ndi gwero la zoipa zonse. Chifukwa cha kuika mtima pa ndalama anthu ena adasokera, adasiya njira ya chikhulupiriro, ndipo adadzitengera zoŵaŵitsa mitima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti kukonda ndalama ndiye muzu wa zoyipa za mitundu yonse. Anthu ena ofunitsitsa ndalama, asochera ndipo asiya njira yachikhulupiriro ndipo adzitengera zowawitsa zambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo cikondi ca pa ndalama; cimene ena pocikhumba, anasocera, nataya cikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.