1 Timothy 6:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma iwe, munthu wa Mulungu, uzipewe zonsezi. Uzikhala ndi mtima wofunafuna chilungamo, wolemekeza Mulungu, wokhulupirika, wachikondi, wolimbika ndi wofatsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iwe, munthu wa Mulungu, thawa zinthu zonsezi. Tsatira chilungamo, moyo wolemekeza Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, kupirira ndi kufatsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate cilungamo, cipembedzo, cikhulupiriro, cikondi, cipiriro, cifatso.