1 Timothy 6:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amene ali olemera pa zinthu zapansipano, uŵalamule kuti asanyade kapena kudalira chuma chimene sichidziŵika ngati chidzakhalitsa. Koma azidalira Mulungu amene amatipatsa zonse moolowa manja kuti tisangalale nazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Lamulira iwo achuma m'nthawi yino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onse amene ali ndi chuma uwalamule kuti asanyade kapena kuyika mitima yawo pa chuma chimene nʼchosadalirika. Koma chiyembekezo chawo chikhale mwa Mulungu amene amatipatsa mowolowamanja zonse zotisangalatsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Lamulira iwo acuma m'nthawi yino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere cuma cosadziwika kukhala kwace, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kocurukira, kuti tikondwere nazo;