1 Timothy 6:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amene ambuye ao ndi akhristu, asaŵapeputse poona kuti ndi abale. Kwenikweni aziŵatumikira koposa, popeza kuti amene amapindula ndi ntchito yao, nawonso ndi akhristu, ndiponso okondedwa. Uziŵaphunzitsa anthu ndi kuŵalamula ntchito zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo akukhala nao ambuye okhulupirira, asawapeputse popeza ali abale; koma makamaka awatumikire popeza ali okhulupirira ndi okondedwa, oyanjana nao pa chokomacho. Izi uphunzitse, nuchenjeze.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amene ambuye awo ndi okhulupirira, asawapeputse chifukwa ambuye ndi abale mʼchikhulupiriro. Mʼmalo mwake akuyenera kuwatumikira bwino chifukwa ambuye wawo ndi okondedwa monga okhulupirira ndiponso ndi odzipereka kusamalira akapolo awo. Zinthu izi ukuyenera kuziphunzitsa ndi kuwalamula anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo akukhala nao ambuye okhulupira, asawapeputse popeza ali abale; koma makamaka awatumikire popeza ali okhulupira ndi okondedwa, oyanjana nao pa cokomaco, Izi uphunzitse, nucenjeze.