1 Timothy 6:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe Timoteo, usunge bwino zimene adakusungitsa. Upewe nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, ndiponso maganizo otsutsana, amene anthu amanama kuti ndi nzeru zodziŵa zinthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Timoteo iwe, dikira chokusungitsa, ndi kulewa zokamba zopanda pake ndi zotsutsana za ichi chitchedwa chizindikiritso konama;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Timoteyo, samalitsa zimene unapatsidwa. Upewe nkhani zopanda pake zosalemekeza Mulungu ndiponso maganizo otsutsana amene amaganizidwa molakwika kuti ndi nzeru.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Timoteo iwe, dikira cokusungitsa, ndi kulewa zokamba zopanda pace ndi zotsutsana za ici cichedwa cizindikiritso konama;