1 Timothy 6:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wotere ndi wodzitukumula ndi kunyada, sadziŵa kanthu. Mtima wake ngwodwala, wongofuna zotsutsanatsutsana ndi kukangana pa mau chabe. Zimenezi zimabweretsa kaduka, kusamvana, kusinjirirana, kuganizirana zoipa,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
iyeyo watukumuka, wosadziwa kanthu, koma ayalukira pa mafunso ndi makani a mau, kumene zichokerako njiru, ndeu, zamwano, mayerekezo oipa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ameneyo ndi wodzitukumula ndipo sakudziwa chilichonse. Iyeyo ali ndi maganizo oyipa, wokonda kusemphana mawu ndi kutsutsana. Zimenezi zimabweretsa nsanje, mikangano, mʼnyozo, kuganizirana zoyipa,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
iyeyo watukumuka, wosadziwa kanthu, koma ayarukira pa mafunso ndi makani a mau, kumene zieokerako njiru, ndeu, zamwano, mayerekezo oipa;