2 Chronicles 1:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adamuyankha kuti, “Chifukwa chakuti waganiza zimenezi mumtima mwako, ndipo sudapemphe katundu, chuma, ulemu, kapena imfa ya adani ako, sudadzipempherenso moyo wautali, koma wapempha nzeru ndi luntha, kuti uzilamulira anthu anga amene ndakulongera ufumu, chabwino
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anati kwa Solomoni, Popeza chinali mumtima mwako ichi, osapempha chuma, akatundu, kapena ulemu, kapena moyo wa iwo akudana nawe, osapemphanso masiku ambiri; koma wadzipemphera nzeru ndi chidziwitso, kuti uweruze anthu anga amene ndakuika ukhale mfumu yao,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu anati kwa Solomoni, “Popeza izi ndi zokhumba za mtima wako ndipo sunapemphe katundu, chuma kapena ulemu, kapena imfa ya adani ako, ndiponso poti sunapemphe moyo wautali koma nzeru ndi luntha kuti ulamulire anthu anga amene Ine ndakuyika kukhala mfumu yawo,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anati kwa Solomo, Popeza cinali mumtima mwako ici, osapempha cuma, akatundu, kapena ulemu, kapena moyo wa iwo akudana nawe, osapemphanso masiku ambiri; koma wadzipemphera nzeru ndi cidziwitso, kuti uweruze anthu anga amene ndakuika ukhale mfumu yao,