2 Chronicles 1:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adasonkhanitsa magaleta ndiponso anthu okwera pa akavalo. Magaletawo anali nawo 1,400, anthu okwera pa akavalo analipo 12,000. Adaŵakhazika ena ku mizinda yokhalako ankhondo ena pafupi ndi mfumu ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi apakavalo, nakhala nao magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'midzi ya magaleta ndi kwa mfumu ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi akavalo; anali ndi magaleta 1,400 ndi akavalo 12,000, amene anawayika mʼmizinda yosungira magaleta ndipo ena anali ndi iye mu Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Solomo anasonkhanitsa magareta ndi apakavalo, nakhala nao magareta cikwi cimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'midzi ya magareta ndi kwa mfumu ku Yerusalemu.