2 Chronicles 1:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mu Yerusalemumo mfumu idasandutsa siliva ndi golide kukhala wambiri ngati miyala wamba. Adasandutsanso mkungudza kukhala wochuluka ngati mikuyu ya m'zigwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inatero kuti siliva ndi golide zikhale m'Yerusalemu ngati miyala, ndi kuti mikungudza ichuluke ngati mikuyu yokhala kuchidikha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inasandutsa siliva ndi golide kukhala ngati miyala wamba mu Yerusalemu. Inasandutsanso mkungudza kukhala wochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya ku zigwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inatero kuti siliva ndi golidi zikhale m'Yerusalemu ngati miyala, ndi kuti mikungudza icuruke ngati mikuyu yokhala kucidikha.