2 Chronicles 1:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo ankagula galeta ku Ejipito pa mtengo wa masekeli asiliva 600 ndipo kavalo pa mtengo wa ndalama zasiliva 150. Momwemonso mafumu onse a Ahiti ndi a ku Siriya nawonso ankagula zinthu kudzera mwa anthu amalonda omwewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatenga natuluka nalo galeta ku Ejipito mtengo wake masekeli a siliva mazana asanu ndi limodzi, ndi kavalo mtengo wake zana limodzi mphambu makumi asanu; momwemo anawatulutsira mafumu onse a Ahiti, ndi mafumu a Aramu, ndi dzanja lao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ankagula galeta ku Igupto pa mtengo wa masekeli asiliva 600 ndipo kavalo pa mtengo wa ndalama zasiliva 150. Iwo ankazigulitsanso kwa mafumu onse a Ahiti ndi a Aramu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatenga naturuka nalo gareta ku Aigupto mtengo wace masekeli a siliva mazana asanu ndi limodzi, ndi kavalo mtengo wace zana limodzi mphambu makumi asanu; momwemo anawaturutsira mafumu onse a Ahiti, ndi mafumu a Aramu, ndi dzanja lao.