2 Chronicles 1:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Solomoni pamodzi ndi anthu onse amene adasonkhana nawo, adapita ku kachisi wa ku Gibiyoni. Paja chihema chamsonkhano cha Mulungu chimene Mose, mtumiki wa Chauta, adaamanga ku chipululu chinali kumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Solomoni ndi khamu lonse pamodzi naye anamuka ku msanje wa ku Gibiyoni; pakuti kumeneko kunali chihema chokomanako cha Mulungu adachimanga Mose mtumiki wa Yehova m'chipululu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni pamodzi ndi gulu lonse la anthu anapita ku malo ofunika kwambiri pachipembedzo ku Gibiyoni. Tenti ya msonkhano ya Mulungu inali kumeneko, imene Mose mtumiki wa Yehova anayipanga mʼchipululu muja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Solomo ndi khamu lonse pamodzi naye anamuka ku msanje wa ku Gibeoni; pakuti kumeneko kunali cihema cokomanako ca Mulungu adacimanga Mose mtumiki wa Yehova m'cipululu.